Exodus 15:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzaŵaloŵetsa ndi kuŵakhazika pa phiri lanu, pa malo amene Inu Chauta mudaŵapanga kuti akhale anu, m'nyumba yopembedzera imene Inu mudaimanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka pa phiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa pa phiri lanu. Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo; malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka pa phiri la colowa canu, Pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, Malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.