Exodus 15:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene akavalo a Farao, pamodzi ndi magaleta ndi okwerapo ake omwe, adaloŵa m'nyanja, Chauta adaŵabweza madziwo, ndipo adamiza onsewo. Koma Aisraele adayenda pouma m'kati mwa nyanjayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magaleta ake ndi apakavalo ake, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israele anayenda pouma pakati pa nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti akavalo a Farao analowa m'nyanja, ndi magareta ace ndi apakavalo ace, ndipo Yehova anawabwezera madzi a m'nyanja; koma ana a Israyeli anayenda pouma pakati pa nyanja.