Exodus 15:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Miriyamu, mneneri wamkazi, mlongo wa Aroni, adatenga kang'oma, ndipo akazi onse adamtsata pambuyo akuimba ting'oma, ndi kumavina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Miriyamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lake; ndipo akazi onse anatuluka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Miriamu mneneri wamkazi, mlongo wa Aaroni anatenga zoyimbira ndipo akazi onse anamutsatira pambuyo, akuyimba ndi zoyimbira ndi kuvina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Miriamu mneneriyo, mlongo wa Aroni, anagwira lingaka m'dzanja lace; ndipo akazi onse anaturuka kumtsata ndi malingaka ndi kuthira mang'ombe.