Exodus 16:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraele ataona tinthuto sadatidziŵe kuti nchiyani, mwakuti adayamba kufunsana kuti “Kodi timeneti ntiyani?” Mose adaŵauza kuti, “Ameneyu ndi buledi yemwe Chauta wakupatsani kuti mudye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene ana a Israele anakaona, anati wina ndi mnzake, Nchiyani ichi? Pakuti sanadziwe ngati nchiyani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale chakudya chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli atationa anafunsana wina ndi mnzake nati, “Kodi timeneti nʼchiyani?” Popeza sanatidziwe. Mose anawawuza kuti, “Uyu ndi buledi amene Yehova wakupatsani kuti mudye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene ana a Israyeli anakaona, anati wina ndi mnzace, Nciani ici? pakuti sanadziwa ngati nciani. Ndipo Mose ananena nao, Ndiwo mkatewo Yehova wakupatsani ukhale cakudya canu,