Exodus 16:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kukadakhala bwino Chauta akadatiphera ku Ejipito konkuja, kumene tinkakhala tikudya nyama ndi buledi, ndipo tinkakhuta. Koma inu mwatifikitsa kuchipululu kuno kuti mutiphe tonse ndi njala.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena nao ana a Israele, Ha? Mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Ejipito, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife chokhuta; pakuti mwatitulutsa kudza nafe m'chipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kuti, “Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera mʼdziko la Igupto! Kumeneko timadya nyama ndi buledi mpaka kukhuta, koma inu mwabwera nafe ku chipululu kudzapha mpingo wonsewu ndi njala!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena nao ana a Israyeli, Ha! mwenzi titafa ndi dzanja la Yehova m'dziko la Aigupto, pokhala ife pa miphika ya nyama, pakudya mkate ife cokhuta; pakuti mwatiturutsa kudza nafe m'cipululu muno kudzapha msonkhano uwu wonse ndi njala.