Exodus 16:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose adati, “Chauta walamula kuti ‘Musungeko mana ena kuti zidzukulu zanu zidzaone chakudya chimene ndidakupatsani m'chipululu, nditakutulutsani ku Ejipito kuja.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'chipululu, muja ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anati, “Chimene Yehova walamula ndi ichi: ‘Tengani muyeso wa malita awiri a mana ndi kusungira mibado imene ikubwera, kuti iwo adzaone chakudya chimene Ine ndinakupatsani kuti mudye mʼchipululu pamene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati, Awa ndi mau anauza Yehova, Dzazani omeri nao, asungikire mibadwo yanu; kuti aone mkatewo ndinakudyetsani nao m'cipululu, muja ndinakuturutsani m'dziko la Aigupto.