Exodus 16:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aisraelewo adakhala alikudya mana zaka makumi anai, mpaka adakafika kudziko kokhala anthu. Adadya mana mpaka adafika ku malire a dziko la Kanani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aisraeli anadya mana zaka 40, mpaka pamene anafika ku dziko kumene amati akakhazikeko. Iwo anadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a Kanaani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli anadya mana zaka makumi anai, kufikira atalowa dziko la midzi; anadya mana kufikira analowa malire a dziko la Kanani.