Exodus 16:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Mose adati, “Ndi Chauta amene adzakupatsani madzulo nyama yoti mudye, ndi m'maŵa buledi woti nkukhuta, chifukwa choti wamva madandaulo anu onse omuŵiringulira aja. Ife ndife yani? Madandaulo anu simudaŵiringulire ife ai, koma Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife chiyani? Simulikudandaulira ife koma Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anati, “Yehova adzakupatsani nyama madzulo aliwonse ndi buledi mmawa uliwonse kuti mukhute chifukwa Iye wamva madandawulo anu. Nanga ife ndi yani? Kudandaula kwanu simudandaulira ife, koma Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanenanso Mose, Pakukupatsani Yehova nyama ya kudya madzulo, ndi mkate wokhuta m'mawa, atero popeza Yehova adamva madandaulo anu amene mumdandaulira nao. Koma ife ndife ciani? simulikudandaulira ife koma Yehova.