Exodus 17:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono manja a Mose atatopa, Aroni pamodzi ndi Huri uja adatenga mwala namkhazikira Mose kuti akhalepo. Aŵiriwo adakhala wina uku wina uku, atagwirira manja a Mose aja. Adaŵagwirira ndithu mpaka dzuŵa kuloŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Manja a Mose atatopa, Aaroni ndi Huri anatenga mwala ndi kuyika pansi ndipo Mose anakhalapo. Aaroni ndi Huri anagwirizitsa manja a Mose wina mbali ina winanso mbali ina. Choncho manja a Mose analimba mpaka kulowa kwa dzuwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ace, wina mbali yina, wina mbali yina; ndi manja ace analimbika kufikira litalowa dzuwa.