Exodus 17:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Zimenezi muzilembe m'buku kuti zidzakumbukike, ndipo munene pamaso pa Yoswa kuti Aamalekewo adzafafanizika kwathunthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba izi mʼbuku kuti zidzakumbukirike ndipo uwonetsetse kuti Yoswa amve zimenezi, chifukwa Ine ndidzafafaniziratu Amaleki pa dziko lapansi, kotero kuti palibe amene adzawakumbukire.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ici m'buku, cikhale cikumbutso, nucimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse cikumbukilo ca Amaleki pansi pa thambo.