Exodus 17:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye anthuwo adayamba kukangana ndi Mose, namanena kuti, “Tipatseni madzi akumwa.” Mose adaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukuyesa Chauta?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe. Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero iwo anakangana ndi Mose nati, “Tipatse madzi akumwa.” Mose anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukumuyesa Yehova?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe, Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?