Exodus 17:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu aja anali ndi ludzu loopsa, ndipo ankangoŵiringulira Mose, kuti “Chifukwa chiyani mudatitulutsa ku Ejipito kuti mutiphe ndi ludzu, ife pamodzi ndi ana athu ndi zoŵeta zathu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kuchokera ku Ejipito, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kucokera ku Aigupto, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?