Exodus 17:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidzakhala patsogolo pako kumeneko pafupi ndi thanthwelo, pa phiri la Horebu. Ukamenye thanthwe, tsono mudzatuluka madzi m'thanthwemo, kuti anthuwo amwe.” Mose adachitadi zimenezo pamaso pa atsogoleri a Aisraele aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndidzayima patsogolo pako pafupi ndi thanthwe la ku Horebu. Ukamenye thanthwelo, madzi adzatuluka kuti anthu amwe.” Motero Mose anachita zimenezi pamaso pa akuluakulu a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebe; ndipo upande thanthwe, nadzaturukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anacita comweco pamaso pa akuru a Israyeli.