Exodus 17:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malowo adaŵatcha Mayeso ndiponso Makangano, chifukwa Aisraele adakangana ndi Mose, ndipo adayesa Chauta pofunsa kuti, “Kodi Chauta ali nafe, kapena ai?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatcha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, chifukwa cha kutsutsana kwa ana a Israele; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, “Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, cifukwa ca kutsutsana kwa ana a Israyeli; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?