Exodus 17:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adauza Yoswa kuti, “Tisankhulireko amuna ena, maŵa mupite kukamenyana nawo nkhondo Aamaleke. Ine ndidzaimirira pamwamba pa phiri, nditagwira ndodo adandipatsa Mulungu ija.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anati kwa Yoswa, “Sankha amuna amphamvu ndipo upite ukamenyane ndi Amaleki. Mawa ndidzayima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nuturuke kuyambana naye Amaleki; mawa ndidzaima pamwamba pa citunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.