Exodus 18:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yetero, wansembe wa ku Midiyani, mpongozi wake wa Mose, adamva zonse zija zimene Mulungu adachitira Mose ndiponso anthu ake Aisraele. Adamvanso za m'mene Chauta adaŵatulutsira ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yetero, wansembe wa Midiyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adachitira Mose ndi Israele anthu ake, kuti Yehova adatulutsa Israele m'Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yetero wansembe wa ku Midiyani amenenso anali mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake a Aisraeli ndi mmene Yehova anawatulutsira mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yetero, wansembe wa Midyani, mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu adacitira Mose ndi Israyeli anthu ace, kuti Yehova adaturutsa Israyeli m'Aigupto.