Exodus 18:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake Mose adayamba kuweruza milandu ya anthu. Ndipo anthuwo ankabwera ndi milandu yao kwa Moseyo kuyambira m'maŵa mpaka usiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunatero kuti m'mawa mwake Mose anakhala pansi kuweruzira anthu milandu yao; ndipo anthu anakhala chilili pamaso pa Mose kuyambira m'mawa kufikira madzulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunatero kuti m'mawa mwace Mose anakhala pansi kuweruzira anthu mirandu yao; ndipo anthu anakhala ciriri pamaso pa Mose kuyambira m'mawa kufikira madzulo.