Exodus 18:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yetero mpongozi wake wa Mose ataona zonse zimene Moseyo ankachita, adafunsa kuti, “Kodi zonse zimene mukuchitira anthuzi nzotani? Chifukwa chiyani mukukhala nokha pano, pamene anthu akubwerabe kwa inu kuyambira m'maŵa mpaka usiku?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene mpongozi wake wa Mose anaona zonsezi iye anawachitira anthu, anati, Chinthu ichi nchiyani uwachitira anthuchi? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala chilili pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene mpongozi wace wa Mose anaona zonsezi iye anawacitira anthu, anati, Cinthu ici nciani uwacitira anthuci? Umakhala pa wekha bwanji, ndi anthu onse amakhala ciriri pamaso pako kuyambira m'mawa kufikira madzulo?