Exodus 18:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo ndiwo aziweruza anthu nthaŵi zonse. Azibwera ndi milandu yovuta yokha kwa inu, koma timilandu ting'onoting'ono aziweruza okha. Adzakuchepetserani ntchito iwowo pakusenza katunduyo pamodzi nanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo iwo aweruze mirandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti mirandu yaikuru yonse abwere nayo kwa iwe; koma mirandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakucepera nchito, ndi iwo adzasenza nawe.