Exodus 18:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adasankha anthu anzeru pakati pa Aisraelewo ndi kuŵaika kuti akhale atsogoleri a anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anasankha amuna amtima mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anasankha amuna amtima mwa Aisrayeli onse, nawaika akuru a pa anthu, akuru a pa zikwi, akuru a pa mazana, akuru a pa makumi asanu, ndi akuru a pa makumi.