Exodus 18:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwana wake wachiŵiri Mose adaamutcha Eliyezere, (chifukwa adati, “Mulungu wa atate anga ndiye thandizo langa, ndipo adandipulumutsa ku lupanga la Farao.”)
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi dzina la mnzake ndiye Eliyezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mwana wake wachiwiri anamupatsa dzina loti Eliezara, pakuti anati, “Mulungu wa makolo anga anali thandizo langa. Iye anandipulumutsa ku lupanga la Farao.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi dzina la mnzace ndiye Eliezere; pakuti anati, Mulungu wa kholo langa anakhala thandizo langa nandilanditsa ku lupanga la Farao.