Exodus 18:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Mose adamufotokozera zonse zimene Chauta adamchita Farao ndi Aejipito chifukwa cha Aisraelewo. Adamsimbiranso za mavuto omwe adaakumana nawo pa njira, ndi zonse zimene Chauta adaachita poŵapulumutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wake zonse Yehova adazichitira Farao ndi Aejipito chifukwa cha Israele; ndi mavuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anafotokozera mpongozi wace zonse Yehova adazicitira Farao ndi Aaigupto cifukwa ca Israyeli; ndi mabvuto onse anakomana nao panjira, ndi kuti Yehova adawalanditsa.