Exodus 19:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uŵalembere malire anthuwo pozungulira phirilo, ndipo uŵauze kuti, ‘Samalani, musakwere phiri kapena kukhudza tsinde lake. Wina aliyense akalikhudza, afa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzichenjera musakwere m'phiri, musakhudza chilekezero chake; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, ‘Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ukalembere anthu malire pozungulira, ndi kuti, Muzicenjera musakwere m'phiri, musakhudza cilekezero cace; wokhudza phirilo adzaphedwa ndithu;