Exodus 19:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina aliyense asakhudze munthuyo, koma anthu amponye miyala kapena kumubaya. Chikhale choŵeta, chidzaphedwa; akhale munthu, adzaphedwanso. Mbetete ikamalira, anthu abwere ku phiri.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
dzanja lililonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale choweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lake azikwera m'phirimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndi miyala kapena kumulasa ndi mivi. Palibe amene adzamukhudze. Palibe munthu amene adzaloledwa kukhala ndi moyo ngakhale nyama. Iwo adzayenera kuphedwa.’ Koma anthu adzapita ku phirilo akadzamva kulira kwa lipenga la nyanga yankhosa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
dzanja liri lonse lisalikhudze, wakulikhudza azimponyatu miyala, kapena kumpyoza; ngakhale coweta ngakhale munthu, zisakhale ndi moyo. Pamene lipenga libanika liu lace azikwera m'phirimo.