Exodus 19:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adatsika phiri, nakafika kwa anthuwo, ndipo adaŵayeretsa. Anthuwo adachapadi zovala zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anatsika m'phiri kunka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zovala zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Mose anatsika phiri lija nafika kwa anthu aja ndi kuwayeretsa. Iwo anachapa zovala zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anatsika m'phiri kumka kwa anthu, nawapatulitsa anthu; natsuka iwo zobvala zao.