Exodus 19:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono m'maŵa, pa tsiku lakelo, panali mabingu ndi mphezi paphiripo. Kunalinso mtambo wochindikira, ndiponso kulira kwakukulu kwa mbetete. Anthu onse m'mahemamo ankangonjenjemera ndi mantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmamawa wa tsiku lachitatu kunali mabingu, ziphaliwali ndi mtambo wakuda umene unaphimba phiri, ndiponso lipenga lolira kwambiri. Aliyense ku misasa kuja ananjenjemera ndi mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali tsiku lacitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.