Exodus 19:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Phiri lonse la Sinai lidaphimbidwa ndi utsi, chifukwa choti Mulungu adaatsikira paphiripo. Utsiwo unkangokwera ngati utsi wam'ng'anjo, ndipo anthu onse aja ankangonjenjemera kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wake unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Phiri la Sinai linakutidwa ndi utsi, chifukwa Yehova anatsika ndi moto pa phiripo. Utsi unakwera ngati wochokera mʼngʼanjo yamoto ndipo phiri lonse linagwedezeka kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo phiri la Sinai linafuka monsemo, popeza Yehova anatsikira m'moto pamenepo; ndi utsi wace unakwera ngati utsi wa m'ng'anjo, ndi phiri lonse linagwedezeka kwambiri,