Exodus 19:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mose adayankha Chauta kuti, “Anthuwo sangakwere ai, chifukwa mudachenjezeratu kuti, ‘Mulembe malire kuzungulira phirilo, ndipo mulipatule kuti likhale loyera.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m'phiri la Sinai; pakuti Inu mwatichenjeza, ndi kuti, Lemba malire m'phirimo, ndi kulipatula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anati kwa Yehova, “Anthu sangakwere phiri la Sinai chifukwa inu munatichenjeza. Lembani malire kuzungulira phiri ndipo mulipatule kuti likhale loyera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati kwa Yehova, Anthu sangathe kukwera m'phiri la Sinai; pakuti Inu mwaticenjeza, ndi kuti, Lemba malire m'phirimo, ndi kulipatula.