Exodus 19:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Mudaona zimene ndidaŵachita Aejipito, ndiponso muja ndidakunyamulani monga m'mene mphungu imanyamulira ana ake pa mapiko ake, ndipo ndidakufikitsani kwa Ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu munaona chimene ndinachitira Aejipito; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu munaona cimene ndinacitira Aaigupto; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa Ine ndekha.