Exodus 19:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo inu mudzakhala anthu onditumikira Ine ngati ansembe, ndiponso ngati mtundu woyera. Tsono ukaŵauze mau ameneŵa Aisraele.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
inu mudzakhala ansembe achifumu ndi mtundu woyera mtima. Awa ndi mawu amene uyenera kuwawuza Aisraeli.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika. Awa ndi mau amene ukalankhule ndi ana a lsrayeli.