Exodus 2:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwana uja atakula adakampereka kwa mwana wa Farao, ndipo adasanduka mwana wake ndithu. Mwana wa Faraoyo adamutcha Mose, chifukwa adati, “Ndidamuvuula m'madzi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wake. Ndipo anamutcha dzina lake Mose, nati, Chifukwa ndinamvuula m'madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwanayo atakula anakamupereka kwa mwana wa Farao ndipo anakhala mwana wake. Iye anamutcha dzina lake Mose, popeza anati, “Ndinamuvuwula mʼmadzi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo atakula mwanayo, anapita naye kwa mwana wamkazi wa Farao, ndipo iye anakhala mwana wace. Ndipo anamucha dzina lace Mose, nati, Cifukwa ndinambvuula m'madzi.