Exodus 2:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Mose, atakula ndithu, adapita kukacheza kwa anthu a mtundu wake uja, ndipo adaona m'mene ankaŵagwiritsira ntchito moŵazunza kwambiri. Adaona Mwejipito wina akumenya Muhebri, mmodzi mwa anthu a mtundu wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anatulukira kukazonda abale ake, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu Mwejipito ali kukantha Muhebri, wa abale ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lina, Mose atakula, anapita kumene kunali anthu a mtundu wake ndipo anawaona akugwira ntchito yowawa. Iye anaona Mwigupto akumenya Mhebri, mmodzi mwa anthu a mtundu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali masiku amenewo, atakula Mose, kuti anaturukira kukazonda abale ace, napenya akatundu ao; ndipo anaona munthu M-aigupto ali kukantha Mhebri, wa abale ace.