Exodus 2:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Mose atayang'ana uku ndi uku, naona kuti kulibe anthu, adamupha Mwejipitoyo, nafotsera mtembo wake mu mchenga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha Mwejipito, namfotsera mumchenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atayangʼana uku ndi uku, naona kuti panalibe wina aliyense, Mose anamupha Mwiguptoyo ndipo anamukwirira mu mchenga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaunguza kwina ndi kwina, ndipo pamene anaona kuti palibe munthu, anakantha M-aigupto, namfotsera mumcenga.