Exodus 2:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'maŵa mwake atabweranso, adaona kuti Ahebri aŵiri akumenyana. Mose adafunsa wolakwayo kuti, “Chifukwa chiyani ukumumenya mnzako?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mawa mwake anatulukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikugwirana; ndipo ananena ndi wochimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmawa mwake Mose anapita ndipo anaona anthu awiri a Chihebri akumenyana. Iye anafunsa amene anali wolakwa kuti, “Chifukwa chiyani ukumenya Mhebri mnzako?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mawa mwace anaturukanso, ndipo, taonani, anthu awiri Ahebri alikugwirana; ndipo ananena ndi wocimwayo, kuti, Umpandiranji mnzako?