Exodus 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye uja adafunsa Mose kuti, “Kodi ndani adakuika kuti uzitilamula ndi kumatiweruza? Kodi ukufuna kundipha monga muja udaphera Mwejipito uja?” Pamenepo Mose adachita mantha kwambiri naganiza mumtima mwake kuti, “Ha, anthu akudziŵa zimene ndidachita zija!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkulu ndi woweruza wathu? Kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha Mwejipito? Ndipo Mose anachita mantha, nanena, Ndithu chinthuchi chadziwika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu uja anati, “Kodi ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza? Kodi ukufuna kundipha monga momwe unaphera Mwigupto uja?” Mose anachita mantha ndipo anati mu mtima mwake, “Chimene ndinachita chija chadziwika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anati, Wakuika iwe ndani ukhale mkuru ndi woweruza wathu? kuteroku ukuti undiphe, monga unamupha M-aigupto? Ndipo Mose anacita mantha, nanena, Ndithu cinthuci cadziwika.