Exodus 2:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Farao atamva, adayesetsa kuti aphe Mose, koma Mose adathaŵa nakakhala ku dziko la Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina adakhala pansi pafupi ndi chitsime.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Farao anachimva ichi, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midiyani; nakhala pansi pachitsime.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao atamva zimenezi anafuna kuti aphe Mose, koma Mose anathawa ndipo anapita kukakhala ku Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina anakhala pansi pafupi ndi chitsime.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Farao anacimva ici, anafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa pankhope pa Farao, nakhala m'dziko la Midyani; nakhala pansi pacitsime.