Exodus 2:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amene anali wansembe ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi aŵiri. Ana aakaziwo adabwera kudzatunga madzi, kuti adzaze m'chomwera nkhosa ndi mbuzi za bambo wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe wa Midiyani anali nao ana akazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimwero kuti amwetse gulu la atate wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe wa ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi awiri. Iwowa anabwera kudzatunga madzi ndi kudzaza mu zomwera kuti amwetse nkhosa za abambo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe wa Midyani anali nao ana akazi asanu ndi awiri, amene anadza kudzatunga madzi; ndipo anadzaza mimweco kuti amwetse gulu la atate wao.