Exodus 2:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Patapita nthaŵi yaitali ndithu, mfumu ya ku Ejipito ija idamwalira. Monsemo Aisraele ankangolira nawo ukapolo wao uja, namapempha chithandizo, ndipo kulira kwao kudamveka kwa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aejipito; ndi ana a Israele anatsitsa moyo chifukwa cha ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungu chifukwa cha ukapolowo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi yonseyo nʼkuti ana a Israeli akulira chifukwa cha ukapolo wawo uja. Iwo anafuwula kupempha thandizo, ndipo kulira kwawoko kunafika kwa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pakupita masiku ambiri aja, idafa mfumu ya Aigupto; ndi ana a Israyeli anatsitsa moyo cifukwa ca ukapolo wao, nalira, ndi kulira kwao kunakwera kwa Mulungucifukwa ca ukapolowo.