Exodus 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sangathe kumubisanso, maiyo adatenga kadengu kabango, nakamata phula. Tsono mwanayo adamuika m'menemo, nakabisa kadenguko pakati pa bango lalitali m'madzi, pafupi ndi chibumi cha mtsinjewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene sanathe kumbisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa nyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sakanathanso kubisidwa, amayi ake anatenga kadengu kopangidwa ndi bango nakamata phula. Kenaka anayika mwanayo mʼmenemo ndi kukamuyika pa mabango mu mtsinje wa Nailo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene sanathe kumbisanso, anamtengera kabokosi kagumbwa, napakapo nkhunga ndi phula; naikamo mwanayo, nakaika pakati pa mabango m'mbali mwa nyanja.