Exodus 2:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ina mwana wamkazi wa Farao adapita kumtsinje komweko kukasamba. Iyeyo anali ndi adzakazi ake, ndipo onsewo ankangoyenda m'mbali mwa mtsinje muja. Tsono mwana wa Farao uja adakaona kadengu kaja m'bangomo, natuma mdzakazi wake kuti akakatenge.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ake anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wake akatenge.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwana wamkazi wa Farao anatsikira kukasamba m'nyanja; ndipo atsikana ace anayendayenda m'mbali mwa nyanja; ndipo iye anaona kabokosi pakati pa mabango, natuma mdzakazi wace akatenge.