Exodus 2:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mlongo wake wa mwanayo adafunsa kuti, “Bwanji ndikakuitanireni mai wachihebri woti akakulerereni mwanayu?” Mwana wa Farao uja adayankha kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mlongo wake ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka mlongo wake wa mwanayo anafunsa mwana wa Farao kuti, “Ndingapite kukakupezerani mmodzi mwa amayi a Chihebri kuti azikakulererani mwanayu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mlongo wace ananena ndi mwana wamkazi wa Farao, Ndipite ine kodi kukuitanirani woyamwitsa wa Ahebri, akuyamwitsireni mwanayo?