Exodus 2:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mwana wa Farao uja adauza maiyo kuti, “Mtengeni mwanayu, mukandilerere, ine ndidzakulipirani.” Motero mai uja adamtenga mwanayo, nakamlera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwana wa Farao anati, “Tengani mwanayu mukandilerere, ndidzakulipirani.” Mayiyo anatenga mwanayo kukamulera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mwana wamkazi wa Farao ananena naye, Pita naye mwana uyu, ndi kundiyamwitsira iye, ndidzakupatsa mphotho yako. Ndipo mkaziyo anatenga mwanayo, namyamwitsa,