Exodus 20:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamaliza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamariza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse ziri m'menemo, napumula tsiku ladsanu ndi ciwiri; cifukwa cace Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.