Exodus 20:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse ankamva mabingu ndi kulira kwa lipenga, namaona mphezi ndi utsi paphiripo, ndipo ankaopa ndi kunjenjemera, ataima kutali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga, ndi phiri lirikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.