Exodus 20:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Usadzipangire fano kapena chithunzi chilichonse chofanizira kanthu kena kalikonse kakumwamba kapena ka pa dziko lapansi, kapenanso ka m'madzi a pansi pa dziko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena cifaniziro ciri conse ca zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi pa dziko;