Exodus 21:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
koma pambuyo pake adzuka nkumayendayenda kunja, ngakhale kuti akuyenda ndi ndodo, munthu amene adammenyayo sadzalangidwa molipsira, koma adzangolipira chifukwa cha nthaŵi yotayika pa bedi ija. Ndipo adzayenera kumsamala ndithu mnzakeyo mpaka atachira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yake, womkanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pake pokha azimbwezera, namchizitse konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kenaka nachira ndi kuyamba kuyenda ndi ndodo kutuluka kunja kwa nyumba yake, ndiye kuti womenya mnzakeyo sadzayimbidwa mlandu. Komabe adzayenera kulipira womenyedwayo chifukwa cha nthawi imene anagona pa bedi ija, ndiponso ayenera kumusala mpaka atachiritsitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
akaukanso, nakayendayenda pabwalo ndi ndodo yace, womkanthayo azikhala womasuka; pakutsotsa pace pokha azimbwezera, namcizitse konse.