Exodus 21:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukagula kapolo wachihebri, adzakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Muzidzammasula pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, iye osalipirapo kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ukagula mnyamata Muhebri, azigwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi; koma chachisanu ndi chiwiri azituluka waufulu chabe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mukagula kapolo wa Chihebri, azikugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri muzimumasula, ndipo asalipire kanthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ukagula mnyamata Mhebri, azigwira nchito zaka zisanu ndi cimodzi; koma cacisanu ndi ciwiri azituruka waufulu cabe.