Exodus 21:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Anthu aamuna akamayambana, ndipo nkupweteka mai wapathupi, maiyo napititsa padera, koma osafa, amene adampwetekayo adzalipira mtengo uliwonse umene mwamuna wa maiyo angadzatchule. Ndipo adzalipira monga momwe anthu oweruza anganenere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amtchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati anthu akumenyana ndi kupweteka mayi woyembekezera, mayiyo napita padera, koma osavulala, wolakwayo ayenera kulipira chilichonse chimene mwamuna wake wa mkaziyo adzalamula ndipo bwalo lamilandu lavomereza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kuphwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza.