Exodus 21:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ng'ombe ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga, iponyedwe miyala, ndipo nyama yake musadye. Koma mwiniwake wa ng'ombeyo asalangidwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yake; koma mwini ng'ombeyo azimasuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati ngʼombe ipha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga yake, iponyedwe miyala ndipo nyama yake isadyedwe. Ndipo mwini ngʼombeyo asayimbidwe mlandu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ng'ombe ikatunga mwamuna kapena mkazi, nafa, aiponyetu miyala ng'ombeyo, osadya nyama yace; koma mwini ng'ombeyo azimasuka.