Exodus 21:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati khalidwe lake la ng'ombeyo linali kumangogunda anthu, ndipo mwiniwake adachenjezedwa, koma iye osaimanga, ng'ombeyo ikapha munthu wamwamuna kapena wamkazi, iponyedwe miyala ndithu. Ndipo mwiniwakeyonso aphedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati ngʼombeyo inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwini wakeyo anachenjezedwa koma iye sanayimange ndipo yapha mwamuna kapena mkazi, ngʼombeyo iponyedwe miyala ndipo mwini wakeyo aphedwenso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamcenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini waceyo amuphenso.